| Chichewa |
|
Zokhudza TBS
Project Baibulo Chichewa
Sakani Malemba
Chipangano Chatsopano
Zokhudza Bungwe la Trinitarian Bible SocietyBungwe la Trinitarian Bible Society linakhazikitsidwa mu chaka cha 1831 monga bungwe logwira ntchito ndi mipingo yosiyanasiyana kuti lipereke kwa anthu kuzungulira dziko lonse lapansi ndi Malemba Oyera okhulupirika ndi olondola, omasulidwa kuchokera ku Malemba a a zilankhulo zabwino kwambiri. Kuyambira mkumano woyambitsa Bungweli mu chaka cha 1831 ife tawona dzanja la Mulungu pa ntchitoyi ndi kudzera mu zosintha zambiri zimene ife takumana nazo. Komabe, chinthu chimodzi chakhala chosasintha kuyambira pa mkumano wokhazikitsa ndicho: cholinga chathu. Cholinga cha Bungweli ndicho kutukula Ulemerero wa Mulungu ndi chipulumutso cha anthu, mwa kusindikiza, kuno ku Ulaya ndi mayiko akunja, podalira pa dalitso la Umulungu, Malemba Oyera, amene aperekedwa mwa kuwuzulidwa kwa Mulungu, ndipo ali ndi kuthekera kwakupangitsa anthu kukhala anzeru ku chipulumutso, mwa chikhulupiriro chimne chili mwa Khristu Yesu. Lero Bungwe la Trinitarian Bible Society liri pa ntchito yotanthawuzira kapena kuchita chibwereza cha Baibulo mu zilankhulo zokwana makumi anayi. Pamene pali kuthekera ife timatanthawuzira kuchokera ku zilankhulo za m’masiku a Baibulo, Chihebri cha “Masoretic” potanthawuzira Chipangano Chakale ndi la Chigriki la Mpukutu Wolandiridwa “Received Text” potanthawuzira Chipangano Chatsopano. Ife timagwiritsa ntchito mfundo ya ndondomeko yofananiza kotero kuti kutanthawuzira kwathu kuli kofanana pafupi kwambiri ndi Malemba owuziridwa mwa umulungu. Pamene kutanthawuzira kapena kubwereza kwamalizika ife timayang’ana pa za kusindikiza ndi kufalitsa Malembawo, monga Ambuye apereka kuthekera. Ife timatukulanso malemba otanthawuzidwa amene ali olondola ndi odalirika. Nthawi zina malemba otanthawuzidwawa akhala okonzedwa ndi Bungwe la Trinitarian Bible Society, nthawi zina anali otanthawuzidwa kuchokera ku mipukutu yabwino kwambiri. Ndipo mu zonsezi, ife tipitirira kugwiritsitsa chiphunzitso cha chi “Protestant” cha Malemba Oyera ndi Utatu Woyera. Kutanthawuzira kwa Malemba a ChichewaMalemba Oyera a mu Chichewa anasindikizidwa koyamba mu chaka cha mzaka za m’ma 1800, kuyambira ndi Uthenga Wabwino malingana ndi Mariko. Chipangano Chatsopano chinatanthawuzidwa pansi pa kuyang’anira kwa “Free Church of Scotland Mission” mu chaka cha 1886. Kutanthawuzira kwatsopano kochitika ndi a Malawi kunasindikizidwa mu chaka cha 2017 ndipo sikuli kolakwika kunena kuti kutanthawizira uku kunagonera pa matanthawuzidwe a Chingerezi a “New International Version”. Bungwe la Trinitarian Bible Society ndi Bungwe la Free Grace Evangelistic Association linalowa mu mgwirizano mu chaka cha 2015 kuti lichite chibwereza ku Chipangano Chatsopano chomwe chilipo. Chibwereza chachikulu ichi chinagonera pa Baibulo la Chingerezi la “King James Verion” mofafaniza ndi Mpukutu wa Chigriki wa “Received Text”. Ntchito yakutanthawuzira yomaliza ya Chipangano Chatsopano inaperekedwa ku Trinitarian Bible Society mu chaka cha 2019 ndipo pambuyo pake kufufuza mosamalitsa kwa malembedwe a Chipangano Chatsopano cha Chichewa kunavomerezedwa kuti pakhale kusindikiza ndi Komiti Yayikulu ya Trinitarian Bible Society. Mu chaka cha 2018 mgwirizano wina unafikiridwa wakuchita chibwereza cha Chipangano Chakale, kuyambira ndi Masalimo ndi Miyambo. Ntchito ya chibwerezayi ikuwoneka kuti yapeza popondera kukonzekera ndi kutanthawuzira Baibulo la Chichewa kuchokera ku Mpukutu weniweni wa Chihebri wa “Masoretic Text” wa Chipangano Chakale ndi Mpukutu wa Chigriki wa “Received Text” wa Chipangano Chatsopano mothandizidwa ndi Bungwe lomwe timagwira nalo ntchito limodzi la “Gereformeerde Bijblestichting”. Kutanthawuzira kwatsopano kudzafananizidwanso ku ma Baibulo amene alipo monga Buku Lopatulika ndi Chipangano Chatsopano – Mpangidwe wa Mfumu Yakob. Pa chifukwa chofuna kugwiritsa ntchito matchulidwe a mawu a umulungu omwe akugwiritsidwa ntchito tsopano ndi ovomerezeka ndi mipingo (kupatula mu malo amene matchulidwe oterowo afunika kukonzedwa). Chifukwa cha kutalika kwa nthawi imene imatengera kuti pakhale kukonza ndi kusindikiza matanthawuzidwe atsopano, ntchito imene ikugwiridwa tsopano ya matanthawuzidwe a chibwereza pogonera pa Baibulo la Chingerezi la “King James Version” inayambidwa kuti ipereke Baibulo lolondola koposa la Mawu a Mulungu kwa olankhula Chichewa mu zaka zochepa chabe. Mapemphero a ntchito ya chibwereza ndi matanthawuzidwe adzafunikira pamene ife tiyesetsa kuti tipereke matanthawuzidwe okhulupirika ndi olondola a Mawu a Mulungu kwa olankhula Chichewa mu Malawi, Mozambique ndi Zambia. Sakani MalembaZikubwera posachedwa. Chipangano ChatsopanoZikubwera posachedwa. |